Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:12

[1] Choncho, lekani zoyipa zonse, chinyengo chilichonse, chiphamaso, nsanje ndi kusinjirira kulikonse.

[2] Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu,

[3] pakuti tsopano mwalawadi kuti Ambuye ndi wabwino.

[4] Pamene mukubwera kwa Iye, amene ndi Mwala wa moyo, umene anthu anawukana, koma Mulungu anawusankha kuti ndi wa mtengowapatali,

[5] inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.

[6] Pakuti mʼMalemba mwalembedwa kuti, “Taonani, ndikuyika mwala wa maziko mu Ziyoni, wosankhika ndi wamtengowapatali. Amene akhulupirira Iye sadzachititsidwa manyazi.”

[7] Tsono kwa inu okhulupirira, mwalawo ndi wamtengowapatali. Koma kwa amene sakhulupirira, “Mwala umene amisiri anawukana wasanduka mwala wa maziko,

[8] ndi “Mwala wopunthwitsa anthu ndiponso thanthwe limene limagwetsa anthu.” Iwo amapunthwa chifukwa samvera uthenga, pakuti ichi ndiye chinali chifuniro cha Mulungu pa iwo.

[9] Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.

[10] Kale simunali anthu ake, koma tsopano ndinu anthu a Mulungu. Kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.

[11] Okondedwa, ndikukupemphani, ngati alendo pansi pano, pewani zilakolako za uchimo, zimene zimachita nkhondo ndi moyo wanu.

[12] Khalani moyo wabwino pakati pa anthu osapembedza kuti ngakhale atakusinjirirani kuti mumachita zoyipa, iwowo akaona ntchito zanu zabwino, adzalemekeza Mulungu pa tsiku lomwe Iye adzatiyendere.

[13] Gonjerani maulamuliro onse chifukwa cha Ambuye. Kaya ndi mfumu, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro waukulu,

[14] kaya ndi mabwanamkubwa, pakuti watumidwa ndi mfumu kuti alange onse amene amachita zoyipa ndi kuyamikira onse amene amachita zabwino.

[15] Pakuti Mulungu akufuna kuti pochita ntchito zabwino muthetse kuyankhula mosazindikira ndi mopusa.

[16] Mukhale monga mfulu, koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo ngati chophimbira zoyipa; mukhale monga atumiki a Mulungu.

[17] Chitirani ulemu aliyense, kondani abale okhulupirira, wopani Mulungu, ndipo chitirani mfumu ulemu.

[18] Inu akapolo, gonjerani ambuye anu ndi kuwachitira ulemu, osati kwa iwo okha amene ndi abwino ndi omvetsa zinthu, komanso kwa amene ndi ankhanza.

[19] Pakuti ndi chinthu chokoma ngati munthu apirira mu zowawa zimene sizinamuyenera chifukwa chodziwa kuti Mulungu alipo.

[20] Kodi pali choti akuyamikireni ngati mupirira pomenyedwa chifukwa choti mwalakwa? Koma ngati mumva zowawa chifukwa chochita zabwino ndi kupirira, mwachita choyamikika pamaso pa Mulungu.

[21] Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake.

[22] “Iye sanachite tchimo kapena kunena bodza.”

[23] Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. Mʼmalo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama.

[24] Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.

[25] Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.

Kalata Yoyamba ya Petro — Chapters